Yeremiya 38:17 - Buku Lopatulika17 Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Ngati mudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mzindawu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Ngati mudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mudziwu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Yeremiya adauza Zedekiya kuti, “Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mzinda uno sadzautentha. Inuyo pamodzi ndi banja lanu mudzakhala moyo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Pamenepo Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mudzakhala ndi moyo ndipo mzinda uno sadzawutentha, inu pamodzi ndi banja lanu mudzakhala ndi moyo. Onani mutuwo |
Ndipo kunali chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri cha kumtenga ndende Yehoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya Babiloni anamuweramutsa mutu wake wa Yehoyakini mfumu ya Yuda atuluke m'kaidi, chaka cholowa iye ufumu wake;