Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 38:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo anamkweza Yeremiya ndi zingwe, namtulutsa m'dzenjemo; ndipo Yeremiya anakhalabe m'bwalo la kaidi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo anamkweza Yeremiya ndi zingwe, namtulutsa m'dzenjemo; ndipo Yeremiya anakhalabe m'bwalo la kaidi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Tsono adamtulutsira kunja ndi zingwe, ndipo Yeremiya adakakhalanso konkuja ku bwalo la alonda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 ndipo anamukoka ndi zingwe ndi kumutulutsa mʼchitsimecho. Ndipo Yeremiya anakhalabe ku bwalo la alonda.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 38:13
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.


ndipo muziti, Itero mfumu, Khazikani uyu m'kaidi, mumdyetse chakudya cha nsautso, ndi madzi a nsautso, mpaka ndikabwera ndi mtendere.


Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene ili kubwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.


Anthu ankhanza ada wangwiro; koma oongoka mtima asamalira moyo wake.


Pamenepo akulu ndi anthu onse anati kwa ansembe ndi kwa aneneri, Munthu uyu sayenera kufa: pakuti watinenera ife m'dzina la Yehova Mulungu wathu.


Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babiloni inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali kunyumba ya mfumu ya Yuda.


Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma kumseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mzinda. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi.


Ndipo Ebedemeleki Mkusi anati kwa Yeremiya, Kulungatu zingwe ndi nsaluzi zotaya zakale ndi zansanza ndi kuzikwapatira. Ndipo Yeremiya anachita chomwecho.


Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi mpaka tsiku lakugwidwa Yerusalemu. Ndipo anali komweko pogwidwa Yerusalemu.


Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.


Ambuye munanenera moyo wanga milandu yake; munaombola moyo wanga.


anati, Ndidzamva mlandu wako, pamene akukunenera afika. Ndipo analamulira kuti amdikire iye m'nyumba ya milandu ya Herode.


Koma zitapita zaka ziwiri Porkio Fesito analowa m'malo a Felikisi; ndipo Felikisi pofuna kukonda Ayuda anamsiya Paulo m'nsinga.


Ndipo pamene tinalowa mu Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikali womdikira iye.


Ndipo anakhala zaka ziwiri zamphumphu m'nyumba yake yobwereka, nalandira onse akufika kwa iye,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa