Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 38:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Ebedemeleki anatenga anthuwo, nalowa nao m'nyumba ya mfumu ya pansi pa nyumba ya chuma, natenga m'menemo nsalu zakale zotaya ndi zansanza zovunda, nazitsitsira ndi zingwe kwa Yeremiya m'dzenjemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Ebedemeleki anatenga anthuwo, nalowa nao m'nyumba ya mfumu ya pansi pa nyumba ya chuma, natenga m'menemo nsalu zakale zotaya ndi zansanza zovunda, nazitsitsira ndi zingwe kwa Yeremiya m'dzenjemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Apo Ebedemeleki adapita ku nyumba ya mfumu ndi anthuwo, nakatenga nsanza m'chipinda cha zovala. Nsanzazo adazitsitsa ndi zingwe m'chitsime m'mene munali Yeremiya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Pamenepo Ebedi-Meleki anatenga anthuwo, napita nawo ku nyumba ya mfumu ya pansi pa chipinda chosungiramo chuma. Kumeneko anakatengako sanza ndipo anatsitsira sanzazo ndi chingwe mʼchitsime mʼmene munali Yeremiya.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 38:11
5 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inamuuza Ebedemeleki Mkusi, kuti, Tenga anthu makumi atatu, umkweze numtulutse Yeremiya mneneri m'dzenjemo, asanafe.


Ndipo Ebedemeleki Mkusi anati kwa Yeremiya, Kulungatu zingwe ndi nsaluzi zotaya zakale ndi zansanza ndi kuzikwapatira. Ndipo Yeremiya anachita chomwecho.


Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.


Ndipo pamene Ebedemeleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m'dzenje; mfumu ilikukhala pa Chipata cha Benjamini;


Koma siliva yense, ndi golide yense, ndi zotengera za mkuwa ndi chitsulo zikhala chopatulikira Yehova; zilowe m'mosungira chuma cha Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa