Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 37:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo Ababiloni adzabweranso, nadzamenyana ndi mzinda uwu; ndipo adzaulanda, nadzautentha ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo Ababiloni adzabweranso, nadzamenyana ndi mudzi uwu; ndipo adzaulanda, nadzautentha ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ndipo Ababiloni adzabwerera kudzathira nkhondo mzinda uno. Adzaugonjetsa ndi kuutentha.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ndipo Ababuloni adzabwerera kudzathira nkhondo mzinda uno. Iwo adzawugonjetsa ndi kuwutentha.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 37:8
9 Mawu Ofanana  

Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mzinda uwu.


ndipo Ababiloni, olimbana ndi mzinda uwu, adzafika nadzayatsa mzindawu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.


Yehova Mulungu wa Israele atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mzindawu m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzautentha ndi moto;


Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Ababiloni akumenyana nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okhaokha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m'hema wake ndi kutentha mzinda uwu ndi moto.


koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.


Ndipo adzatulutsira Ababiloni akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babiloni; ndipo mudzatenthetsa mzindawu ndi moto.


Yehova atero, Mzindawu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa