Yeremiya 37:7 - Buku Lopatulika7 Atero Yehova, Mulungu wa Israele: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakutulukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Ejipito ku dziko lao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Atero Yehova, Mulungu wa Israele: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakutulukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Ejipito ku dziko lao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 “Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti mfumu ya ku Yuda imene idakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa Ine, uiwuze kuti, ‘Gulu lankhondo la Farao limene lidaabwera kuti lidzakuthandize, posachedwa libwerera kwao ku Ejipito, dziko lake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 “Uyiwuze mfumu ya Yuda imene inakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa ine kuti Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, gulu lankhondo la Farao limene linatuluka kuti lidzakuthandize lidzabwerera kwawo ku Igupto. Onani mutuwo |