Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 37:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo nkhondo ya Farao inatuluka mu Ejipito; ndipo pamene Ababiloni omangira misasa Yerusalemu anamva mbiri yao, anachoka ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo nkhondo ya Farao inatuluka m'Ejipito; ndipo pamene Ababiloni omangira misasa Yerusalemu anamva mbiri yao, anachoka ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 M'menemonso nkuti gulu lankhondo la Farao litatuluka ku Ejipito. Ndipo pamene Ababiloni ozinga mzinda wa Yerusalemu ndi zithando zankhondo adamva zimenezo, adachokako ku Yerusalemuko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Nthawi imeneyinso nʼkuti gulu lankhondo la Farao litatuluka mʼdziko la Igupto. Ndipo Ababuloni amene anali atazinga Yerusalemu atamva zimenezi, anachoka ku Yerusalemuko.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 37:5
7 Mawu Ofanana  

Koma mfumu ya Aejipito sinabwerezenso kutuluka m'dziko lake, pakuti mfumu ya Babiloni idalanda kuyambira ku mtsinje wa Ejipito kufikira ku mtsinje Yufurate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aejipito.


Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda ndi akulu ake ndidzawapereka m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la akufuna moyo wao, ndi m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, imene yakuchokerani.


Ndipo panali pamene nkhondo ya Ababiloni inachoka ku Yerusalemu chifukwa cha nkhondo ya Farao,


Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya mneneri, kuti,


Atero Yehova, Mulungu wa Israele: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakutulukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Ejipito ku dziko lao.


Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yake ku Ejipito, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? Adzapulumuka wakuchita izi? Athyole pangano ndi kupulumuka kodi?


Ndipo Farao ndi nkhondo yake yaikulu, ndi khamu lake launyinji, sadzachita pamodzi naye kunkhondo, pakuunda mtumbira, ndi kumanga malinga, kulikha anthu ambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa