Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 37:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Zedekiya mwana wa Yosiya anakhala mfumu m'malo a Koniya mwana wa Yehoyakimu, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni inamlowetsa mfumu m'dziko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Zedekiya mwana wa Yosiya anakhala mfumu m'malo a Koniya mwana wa Yehoyakimu, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni inamlowetsa mfumu m'dziko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adakhazika Zedekiya pa mpando waufumu wa ku Yuda, kuloŵa m'malo mwa Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, inakhazika pa mpando waufumu Zedekiya mwana wa Yosiya kukhala mfumu ya Yuda. Iye analowa mʼmalo mwa Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 37:1
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehoyakini mfumu ya Yuda anatulukira kwa mfumu ya Babiloni, iye ndi make, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi adindo ake; mfumu ya Babiloni nimtenga chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.


Ndipo mfumu ya Babiloni analonga Mataniya mbale wa atate wake akhale mfumu m'malo mwake, nasanduliza dzina lake likhale Zedekiya.


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Zedekiya mfumu anatuma kwa iye Pasuri mwana wa Malikiya, ndi Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, akati,


Pali Ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wake wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya padzanja langa lamanja, ndikadachotsa iwe kumeneko;


Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? Chifukwa chanji atulutsidwa iye, ndi mbeu zake, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa?


Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni.


Yehova Mulungu wa Israele atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mzindawu m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzautentha ndi moto;


Ndipo panali chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha undende wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi iwiri, tsiku la makumi awiri ndi asanu la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babiloni anaweramutsa mutu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, namtulutsa iye m'ndende;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa