Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 36:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo Baruki mwana wa Neriya anachita monga mwa zonse anamuuza iye Yeremiya mneneri, nawerenga m'buku mau a Yehova m'nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo Baruki mwana wa Neriya anachita monga mwa zonse anamuuza iye Yeremiya mneneri, nawerenga m'buku mau a Yehova m'nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Motero Baruki mwana wa Neriya adachita zonse zimene mneneri Yeremiya adamuuza kuti achite. Adaŵerenga mau a Chauta olembedwa m'buku aja m'Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Baruki mwana wa Neriya anachita zonse zimene mneneri Yeremiya anamuwuza kuti achite. Mʼnyumba ya Yehova, iye anawerenga mawu a Yehova ochokera mʼbukulo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 36:8
9 Mawu Ofanana  

Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo.


Koma iwe ukwinde m'chuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.


ndipo ndinapereka kalata yogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamaso pa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata yogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la kaidi.


Ndipo Yeremiya anaitana Baruki mwana wa Neriya; ndipo Yeremiya analembetsa Baruki m'buku lampukutu mau onse a Yehova, amene ananena naye.


koma pita iwe, nuwerenge mu mpukutu umene ndakulembetsa, mau a Yehova m'makutu a anthu m'nyumba ya Yehova tsiku lakusala kudya; ndiponso udzawawerenga m'makutu a Ayuda onse amene atuluka m'mizinda yao.


Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.


Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa