Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 34:4 - Buku Lopatulika

4 Koma tamva mau a Yehova, iwe Zedekiya mfumu ya Yuda; Yehova atero za iwe, Sudzafa ndi lupanga;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma tamva mau a Yehova, iwe Zedekiya mfumu ya Yuda; Yehova atero za iwe, Sudzafa ndi lupanga;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Komabe imva mau a Chauta, iwe Zedekiya mfumu ya ku Yuda. Akuti, Sudzafera pa nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Koma iwe Zedekiya mfumu ya Yuda, imva lonjezo ili la Yehova. Izi ndi zimene Yehova akunena za iwe: Sudzaphedwa pa nkhondo;

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 34:4
7 Mawu Ofanana  

Nati iye, Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lilikuima padzanja lake lamanja, ndi padzanja lake lamanzere.


Tamvani mau a Yehova, iwe nyumba ya Yakobo, ndi inu mabanja onse a nyumba ya Israele;


ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komweko kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse?


ndipo iwe sudzapulumuka m'dzanja lake, koma udzagwiridwadi, nudzaperekedwa m'dzanja lake; ndipo maso ako adzaonana nao a mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzanena nawe pakamwa ndi pakamwa, ndipo udzanka ku Babiloni.


udzafa ndi mtendere; ndipo adzawambika iwe monga anawambika makolo ako, mafumu akale usanakhale iwe; ndipo adzakulirira iwe, kuti, Kalanga ine ambuye! Pakuti ndanena mau, ati Yehova.


Ima m'chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.


Imvani mau a Yehova, inu ana a Israele; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa