Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 34:3 - Buku Lopatulika

3 ndipo iwe sudzapulumuka m'dzanja lake, koma udzagwiridwadi, nudzaperekedwa m'dzanja lake; ndipo maso ako adzaonana nao a mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzanena nawe pakamwa ndi pakamwa, ndipo udzanka ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 ndipo iwe sudzapulumuka m'dzanja lake, koma udzagwiridwadi, nudzaperekedwa m'dzanja lake; ndipo maso ako adzaonana nao a mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzanena nawe pakamwa ndi pakamwa, ndipo udzanka ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Iweyo sudzapulumuka m'manja mwake. Udzagwidwa ndithu ndipo adzakupereka m'manja mwake. Udzamuwona maso ndi maso, ndipo udzalankhula naye pakamwa ndi pakamwa. Tsono adzakutenga kupita nawe ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iweyo sudzapulumuka mʼmanja mwake koma udzagwidwa ndithu ndipo adzakupereka mʼmanja mwake. Udzayiona mfumu ya ku Babuloni maso ndi maso ako ndipo udzayankhula nayo pakamwa ndi pakamwa. Ndipo udzapita ku Babuloni.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 34:3
18 Mawu Ofanana  

Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.


adzanka nazo ku Babiloni, kumeneko zidzakhala, mpaka tsiku limene ndidzayang'anira iwo, ati Yehova; pamenepo ndidzazikweza, ndi kuzibwezera kumalo kuno.


Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzapereka mzindawu m'dzanja la Ababiloni, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzaulanda,


Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mzinda uwu m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,


ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Ababiloni, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;


Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda ndi akulu ake ndidzawapereka m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la akufuna moyo wao, ndi m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, imene yakuchokerani.


Koma tamva mau a Yehova, iwe Zedekiya mfumu ya Yuda; Yehova atero za iwe, Sudzafa ndi lupanga;


pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni.


koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.


Ndipo adzatulutsira Ababiloni akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babiloni; ndipo mudzatenthetsa mzindawu ndi moto.


Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babiloni, ku dziko la Ababiloni; sadzaliona, chinkana adzafako.


Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yake ku Ejipito, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? Adzapulumuka wakuchita izi? Athyole pangano ndi kupulumuka kodi?


Pali Ine, ati Ambuye Yehova, pamalo pokhala mfumu, imene idamchititsa ufumu, imene anapeputsa lumbiro lake, imene anathyola pangano lake, adzafa pamodzi ndi iye pakati pa Babiloni.


Ndipo iwe wolasidwa woipa, kalonga wa Israele, amene lafika tsiku lako, nthawi ya mphulupulu yotsiriza;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa