Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 34:2 - Buku Lopatulika

2 Yehova Mulungu wa Israele atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mzindawu m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzautentha ndi moto;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yehova Mulungu wa Israele atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzautentha ndi moto;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Pita ukauze Zedekiya mfumu ya ku Yuda kuti Chauta akunena kuti Mzinda uwu ndidzaupereka kwa mfumu ya ku Babiloni, ndipo iyeyo adzautentha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Yehova, Mulungu wa Israeli akuti: Pita kwa Zedekiya mfumu ya Yuda ndipo ukamuwuze kuti Yehova akuti mzinda uno ndidzawupereka mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni ndipo adzawutentha ndi moto.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 34:2
14 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iye ndi khamu lake lonse anadzera Yerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga.


natentha nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu; ndi nyumba zonse zazikulu anazitentha ndi moto.


Pakuti ndaika nkhope yanga pa mzinda uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto.


Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mzinda uwu.


adzanka nazo ku Babiloni, kumeneko zidzakhala, mpaka tsiku limene ndidzayang'anira iwo, ati Yehova; pamenepo ndidzazikweza, ndi kuzibwezera kumalo kuno.


Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mzinda uwu m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,


Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo kumzinda uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.


Ndipo adzatulutsira Ababiloni akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babiloni; ndipo mudzatenthetsa mzindawu ndi moto.


Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa