Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 32:36 - Buku Lopatulika

36 Chifukwa chake tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israele, za mzinda umene, munena inu, waperekedwa m'dzanja la mfumu ya Babiloni ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Chifukwa chake tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israele, za mudzi umene, munena inu, waperekedwa m'dzanja la mfumu ya Babiloni ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Anthu ponena za mzinda umenewu akuti udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babiloni utafooka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Komatu zimene Chauta, Mulungu wa Israele akunena ndi izi:

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 “Anthu ponena za mzindawu akuti udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni mwa nkhondo, njala ndi mliri, koma Yehova Mulungu wa Israeli akuti,

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 32:36
11 Mawu Ofanana  

taonani mitumbira, yafika kumzinda kuugwira, ndipo mzinda uperekedwa m'dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha mliri; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona.


Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzapereka mzindawu m'dzanja la Ababiloni, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzaulanda,


Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mzinda uwu m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,


Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,


Chifukwa chake taonani, ndidzamkopa ndi kunka naye kuchipululu, ndi kulankhula naye momkonda mtima.


Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa