Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 32:34 - Buku Lopatulika

34 Koma anaika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aidetse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Koma anaika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aidetse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Adaika mafano ao onyansa m'Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo adaiipitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Iwo anayika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi dzina langa ndipo anayipitsa.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 32:34
15 Mawu Ofanana  

Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hepeziba.


Natulutsa chifanizocho m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nachitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nachipera chikhale fumbi, naliwaza fumbi lake pa manda a ana a anthu.


Ndipo anachotsa milungu yachilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi mu Yerusalemu, nawataya kunja kwa mzinda.


Ndiponso ansembe aakulu onse ndi anthu anachulukitsa zolakwa zao, monga mwa zonyansa zonse za amitundu, nadetsa nyumba ya Yehova, imene anapatula mu Yerusalemu.


Chifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano achilendo, nafukizira m'menemo milungu ina, imene sanaidziwe, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda; nadzaza malo ano ndi mwazi wa osachimwa;


Pakuti mneneri ndi wansembe onse awiri adetsedwa; inde, m'nyumba yanga ndapeza zoipa zao, ati Yehova.


Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka.


Ndipo mwabwerera inu tsopano, ndi kuchita chimene chili cholungama pamaso panga, pakulalikira ufulu yense kwa mnzake; ndipo munapangana pangano pamaso panga m'nyumba imene itchedwa dzina langa;


Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musachitetu chonyansa ichi ndidana nacho.


ndi kudza ndi kuima pamaso panga m'nyumba ino, imene itchedwa dzina langa, ndi kuti, Talanditsidwa; kuti muchite zonyansa izi?


Pakuti ana a Yuda anachita choipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aliipitse.


Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m'chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao aamuna ndi aakazi; chimene sindiwanauze iwo, sichinalowe m'mtima mwanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa