Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 32:30 - Buku Lopatulika

30 Pakuti ana a Israele ndi ana a Yuda anachita zoipa zokhazokha pamaso panga chiyambire ubwana wao, pakuti ana a Israele anandiputa Ine kokhakokha ndi ntchito ya manja ao, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Pakuti ana a Israele ndi ana a Yuda anachita zoipa zokhazokha pamaso panga chiyambire ubwana wao, pakuti ana a Israele anandiputa Ine kokhakokha ndi ntchito ya manja ao, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Chiyambire pa ubwana wao, Aisraele ndi Ayuda akhala akungochita zoipa pamaso panga, nkumandikwiyitsa ndi ntchito zao zoipa,” akutero Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 “Aisraeli ndi Ayuda akhala akuchita zoyipa zokhazokha pamaso panga kuyambira ubwana wawo. Kunena zoona Aisraeli akumandikwiyitsa ndi ntchito zawo zoyipa, akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 32:30
25 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.


Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.


Pakuti Yehova wa makamu, amene anakuoka iwe, wakunenera iwe choipa, chifukwa cha zoipa za nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda, zimene anadzichitira okha pakuutsa mkwiyo wanga m'mene anafukizira Baala.


Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zake, ndi zabwino zake; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa cholowa changa chonyansa.


Ndinanena ndi iwe m'phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvere mau anga.


musatsate milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, musautse mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu; ndingachitire inu choipa.


Koma simunandimvere Ine, ati Yehova; kuti muutse mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu ndi kuonapo choipa inu.


Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvere mau a Yehova Mulungu wathu.


Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka.


Tenga buku lampukutu, nulembe m'menemo mau onse ndanena kwa iwe akunenera Israele, ndi akunenera Yuda, ndi akunenera amitundu onse kuyambira tsiku ndinanena kwa iwe, kuyambira masiku a Yosiya, mpaka lero.


chifukwa cha choipa chao anachichita kuutsa nacho mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu ina, imene sanaidziwe, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu.


popeza muutsa mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu, pofukizira milungu ina m'dziko la Ejipito, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale chitemberero ndi chitonzo mwa amitundu onse a dziko lapansi?


Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi mu Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?


Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.


Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito.


ndipo anachita chigololo iwo mu Ejipito, anachita chigololo mu ubwana wao; pomwepo anthu anasindikiza mawere ao, pomweponso anakhudza nsonga za mawere za unamwali wao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa