Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 32:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mzinda waperekedwa m'manja a Ababiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mudzi waperekedwa m'manja a Ababiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Komabe ngakhale mzindawu udzaperekedwa kwa Ababiloni, Inu Chauta mudandilamula kuti ndigule mundawo pali mboni ziŵiri.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Ngakhale mzindawu udzaperekedwa kwa Ababuloni, komabe Inu Ambuye Yehova, munandiwuza kuti, ‘Gula munda ndi siliva ndipo upereke ndalamazo pali mboni.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 32:25
11 Mawu Ofanana  

Njira yanu inali m'nyanja, koyenda Inu nkumadzi aakulu, ndipo mapazi anu sanadziwike.


Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wake wachifumu.


Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi mliri mwa iwo, mpaka athedwa m'dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo ao.


Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Nyumba ndi minda ndi minda yampesa idzagulidwanso m'dziko muno.


taonani mitumbira, yafika kumzinda kuugwira, ndipo mzinda uperekedwa m'dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha mliri; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona.


Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,


Ndipo minda idzagulidwa m'dziko lino, limene muti, Ndilo bwinja, lopanda munthu kapena nyama; loperekedwa m'dzanja la Ababiloni.


Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.


Chifukwa chake Yehova atero: Simunandimvere Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wake, ndi munthu yense kwa mnzake; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kumliri, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.


Yesu anayankha nati kwa iye, Chimene ndichita Ine suchidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa