Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 30:8 - Buku Lopatulika

8 Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzathyola goli lake pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzathyola goli lake pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku limenelo ndidzathyola goli laukapolo m'khosi mwao, ndidzadula zingwe zoŵamanga. Aisraele sadzakhalanso akapolo a alendo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzathyola goli la ukapolo mʼkhosi mwawo ndipo ndidzadula zingwe zowamanga; Aisraeli sadzakhalanso akapolo a alendo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 30:8
16 Mawu Ofanana  

Anawatulutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa, nadula zomangira zao.


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wake adzachoka pa phewa lako, ndi goli lake pakhosi pako; ndipo goli lidzathedwa chifukwa cha kudzoza mafuta.


Pakuti Yehova adzamchitira chifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israele, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo achilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza kunyumba ya Yakobo.


kuti Ine ndidzathyola Aasiriya m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lake lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphewa pao.


Ndipo padzakhala tsiku loti Yehova adzakupumitsa chisoni chako, ndi nsautso yako, ndi ntchito yako yovuta, imene anakugwiritsa,


Pakuti goli la katundu wake, ndi mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womsautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midiyani.


Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.


Pakuti mitundu yambiri ndi mafumu aakulu adzayesa iwo atumiki ao; ndipo ndidzabwezera iwo monga mwa machitidwe ao, monga mwa ntchito ya manja ao.


Yehova atero kwa ine: Udzipangire zomangira ndi magoli, nuziike pakhosi pako;


Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu aakulu adzamuyesa iye mtumiki wao.


Pamenepo mneneri Hananiya anachotsa goli pa khosi la Yeremiya, nalithyola.


Pita, nunene kwa Hananiya, kuti Yehova atero: Wathyola magoli amtengo; koma udzapanga m'malo mwao magoli achitsulo.


ndipo ndidzabwezeranso kumalo kuno Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi am'nsinga onse a Yuda, amene ananka ku Babiloni, ati Yehova: pakuti ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babiloni.


Ndi ku Tehafinehesi kudzada usana, pakuthyola Ine magoli a Ejipito komweko; ndi mphamvu yake yodzikuza idzalekeka m'menemo; kunena za ilo mtambo udzaliphimba, ndi ana ake aakazi adzalowa undende.


Ndi mitengo yakuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.


Koma tsopano ndidzathyola ndi kukuchotsera goli lake, ndipo ndidzadula zomangira zako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa