Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 30:5 - Buku Lopatulika

5 Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 “Tamva kulira kwankhaŵa, kufuula kwamantha, ndipo palibe mtendere paliponse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 “Yehova akuti: “Ndamva kulira chifukwa cha nkhawa, ndamva kulira kwa mantha popeza palibe mtendere.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 30:5
22 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang'ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m'mitambo yake.


Tonse tibangula ngati zilombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira chiweruziro koma palibe; tiyang'anira chipulumutso koma chili patali ndi ife.


Akufunkha afika pa mapiri oti see m'chipululu; pakuti lupanga la Yehova lilusa kuyambira pa mbali ina ya dziko kufikira kumbali ina; palibe thupi lokhala ndi mtendere.


Mau akufuula abusa, ndi kukuwa mkulu wa zoweta! Pakuti Yehova asakaza busa lao.


Awa ndi mau ananena Yehova za Israele ndi Yuda.


Chifukwa chanji ndachiona? Aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osacheukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.


Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu uchokera kumpoto; ndi mtundu waukulu udzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi.


Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kumvimvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.


Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mzinda ndi amene akhalamo.


Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi mu Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?


Pakuti mau a kulira amveka mu Ziyoni, Tafunkhidwa, tanyazitsidwa, pakuti tasiya dziko, pakuti agwetsa zokhalamo zathu.


Ndipo ndidzasanduliza zikondwerero zanu zikhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'chuuno monse, ndi mpala pamutu uliwonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi chitsiriziro chake ngati tsiku lowawa.


Inde anyoza mafumu, aseka akalonga; aseka linga lililonse; popeza aunjika dothi, nalilanda.


Pakuti taonani, ndiukitsa Ababiloni, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kulowa m'malo mosati mwao, mukhale mwaomwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa