Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 29:3 - Buku Lopatulika

3 anatumiza kalatayo m'dzanja la Elasa mwana wake wa Safani, ndi Gemariya mwana wake wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatuma ku Babiloni kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 anatumiza kalatayo m'dzanja la Elasa mwana wake wa Safani, ndi Gemariya mwana wake wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatuma ku Babiloni kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Yeremiya kalatayo adapatsira Elasa mwana wa Safani, ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya ku Yuda adaaŵatuma ku Babiloni kwa mfumu Nebukadinezara. M'kalatamo adaalembamo kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yeremiya anapatsira kalatayo Eleasa mwana wa Safani ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatumiza kwa Mfumu Nebukadinezara ku Babuloni. Mʼkalatamo analembamo kuti:

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 29:3
11 Mawu Ofanana  

Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawatulukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba mbiri.


Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Akibori mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,


Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m'nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.


ndi Azariya anabala Helezi, ndi Helezi anabala Eleasa,


ndi Salumu anabala Hilikiya, ndi Hilikiya anabala Azariya,


Mfumu niuza Hilikiya, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Abidoni mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,


ndipo Yehoyakimu mfumu anatuma anthu ku Ejipito, Elinatani mwana wake wa Akibori, ndi anthu ena pamodzi ndi iye, anke ku Ejipito;


Koma dzanja la Ahikamu mwana wa Safani linali ndi Yeremiya, kuti asampereke m'manja a anthu kuti amuphe.


Tsononso Elinatani ndi Delaya ndi Gemariya anapembedzera mfumu kuti asatenthe mpukutuwo; koma anakana kumvera.


iwonso anatumiza, namchotsa Yeremiya m'bwalo la kaidi, nampereka iye kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti anke naye kwao; momwemo iye anakhala ndi anthu.


Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israele, ndi pakati pao panaima Yazaniya mwana wa Safani, munthu aliyense ndi mbale yake ya zofukiza m'dzanja lake; ndi fungo lake la mtambo wa zonunkhira linakwera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa