Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 28:9 - Buku Lopatulika

9 Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzachitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzachitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma ngati mneneri alosa za mtendere, zimene walosazo zikachitikadi, pamenepo zidzadziŵika kuti Chauta adamtumadi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma mneneri amene amalosera zamtendere adzadziwika kuti ndi woona ndi kuti watumidwa ndi Yehova ngati zimene wanenera zachitikadi.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 28:9
9 Mawu Ofanana  

Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za mizinda ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.


Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi chilala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno.


Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! Ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.


Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang'onong'ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.


Ndipo analipoletsa pang'ono bala la mwana wamkazi wa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, mtendere; posakhala mtendere.


Ndipo pakuchitika ichi, pakuti chifikadi, pamenepo adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.


Ndipo mukati m'mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mau amene Yehova sananene?


Mneneri akanena m'dzina la Yehova, koma mau adanenawa sachitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanene; mneneriyo ananena modzikuza, musamuope iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa