Yeremiya 28:8 - Buku Lopatulika8 Aneneri amene analipo kale ndisanakhale ine, nimusanakhale inu, ananenera maiko ambiri, ndi mafumu aakulu, za nkhondo, ndi za choipa, ndi za mliri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Aneneri amene analipo kale ndisanakhale ine, nimusanakhale inu, ananenera maiko ambiri, ndi mafumu akulu, za nkhondo, ndi za choipa, ndi za chaola. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Aneneri amene adatsogola kale ankalosa za nkhondo, za njala ndi za mliri, zodzagwera maiko ambiri ndi maufumu otchuka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Kunali aneneri kalelo, ine ndi iwe tisanabadwe. Iwowa analosera za nkhondo, mavuto ndi mliri kuti zidzagwera mayiko ambiri ndi maufumu amphamvu. Onani mutuwo |