Yeremiya 28:4 - Buku Lopatulika4 ndipo ndidzabwezeranso kumalo kuno Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi am'nsinga onse a Yuda, amene ananka ku Babiloni, ati Yehova: pakuti ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babiloni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 ndipo ndidzabweranso kumalo kuno Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi am'nsinga onse a Yuda, amene ananka ku Babiloni, ati Yehova: pakuti ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babiloni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Ndidzambwezanso ku malo ano Yehoyakini, mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda. Ndidzabweza akapolo onse ochokera ku Yuda amene adatengedwa kupita ku Babiloni. Motero ndidzathyola goli laukapolo la mfumu ya ku Babiloni.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Ndidzabweretsanso pa malo pano Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda pamodzi ndi akapolo ena onse ochokera ku Yuda amene anapita ku Babuloni,’ akutero Yehova, ‘chifukwa ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni.’ ” Onani mutuwo |
Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni.