Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 28:13 - Buku Lopatulika

13 Pita, nunene kwa Hananiya, kuti Yehova atero: Wathyola magoli amtengo; koma udzapanga m'malo mwao magoli achitsulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Pita, nunene kwa Hananiya, kuti Yehova atero: Wathyola magoli amtengo; koma udzapanga m'malo mwao magoli achitsulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 “Pita ukamuuze Hananiya mau a Chauta akuti, ‘Iweyo wathyola goli lamtengo, m'malo mwake Ine ndidzaika goli lachitsulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 “Pita, kawuze mneneri Hananiya kuti, ‘Yehova akuti: Iwe wathyola goli lamtengo, mʼmalo mwake Ine ndidzayika goli lachitsulo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 28:13
10 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzetsani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.


Popeza adaswa zitseko zamkuwa, nathyola mipiringidzo yachitsulo.


kumanga mafumu ao ndi maunyolo, ndi omveka ao ndi majerejede achitsulo,


Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzathyolathyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo;


Pakuti sindinawatume iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupirikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.


Yehova atero kwa ine: Udzipangire zomangira ndi magoli, nuziike pakhosi pako;


Goli la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lake; zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvu yanga; Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwagonjetsa.


Aneneri ako anakuonera masomphenya achabe ndi opusa; osawulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako, koma anakuonera manenero achabe ndi opambutsa.


Ndi ku Tehafinehesi kudzada usana, pakuthyola Ine magoli a Ejipito komweko; ndi mphamvu yake yodzikuza idzalekeka m'menemo; kunena za ilo mtambo udzaliphimba, ndi ana ake aakazi adzalowa undende.


chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa