Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 27:21 - Buku Lopatulika

21 inde, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 inde, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Zoonadi, ameneŵa ndiwo mau a Chauta Wamphamvuzonse onena za ziŵiya zimene zidatsala m'Nyumba ya Chauta, m'nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndiponso mu Yerusalemu, akuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena za zinthu zimene zinatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi mu Yerusalemu kuti,

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 27:21
9 Mawu Ofanana  

Taonani, akudza masiku kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kunka ku Babiloni, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova.


Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikulu ndi zazing'ono, ndi chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha mfumu, ndi cha akalonga ake, anabwera nazo zonsezi ku Babiloni.


Zipangizo zonse zagolide ndi zasiliva ndizo zikwi zisanu ndi mazana anai. Izi zonse Sezibazara anakwera nazo, pokwera andende aja kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu.


Kirusi mfumu anatulutsanso zipangizo za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adazitulutsa mu Yerusalemu, ndi kuziika m'nyumba ya milungu yake;


Taona, masiku afika, kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zimene atate wako anazikundika kufikira lero lino, zidzatengedwa kunka ku Babiloni; sipadzatsala kanthu, ati Yehova.


Ndiponso ndidzapereka chuma chonse cha mzinda uwu, ndi zaphindu zake zonse, ndi zinthu zake zonse za mtengo wake, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m'manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babiloni.


zimene sanazitenge Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, pamene anamtenga ndende Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Babiloni; ndi akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu;


adzanka nazo ku Babiloni, kumeneko zidzakhala, mpaka tsiku limene ndidzayang'anira iwo, ati Yehova; pamenepo ndidzazikweza, ndi kuzibwezera kumalo kuno.


Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse; pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika, amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa