Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 27:19 - Buku Lopatulika

19 Pakuti Yehova wa makamu atero, za zoimiritsa, ndi za thawale, ndi za zoikirapo, ndi za zipangizo zotsala m'mzinda uwu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Pakuti Yehova wa makamu atero, za zoimiritsa, ndi za thawale, ndi za zoikirapo, ndi za zipangizo zotsala m'mudzi uwu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Chauta Wamphamvuzonse ndiye akunena za mizati, chimbiya, maphaka ndi ziŵiya zonse zimene zidatsala mumzindamu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Pakuti Yehova akunena za zipilala, za mbiya ya madzi, maphaka ndi ziwiya zina zimene zatsala mu Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 27:19
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwake kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wake unali mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizungulira.


Ndipo anapanga maphaka khumi amkuwa, m'litali mwake mwa phaka limodzi mikono inai, ndi msinkhu wake mikono itatu.


Ndipo zoimiritsa zamkuwa zinali m'nyumba ya Yehova, ndi maphaka ake, ndi thawale lamkuwa, zinali m'nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, natenga mkuwa wake kunka nao ku Babiloni.


Msinkhu wake wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pake mutu wamkuwa; ndi msinkhu wake wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzake inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.


Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikulu ndi zazing'ono, ndi chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha mfumu, ndi cha akalonga ake, anabwera nazo zonsezi ku Babiloni.


Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse; pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika, amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.


Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa