Yeremiya 27:16 - Buku Lopatulika16 Ndiponso ndinanena kwa ansembe ndi kwa anthu onsewa, kuti, Yehova atero: Musamvere mau a aneneri anu amene akunenerani inu, kuti, Taonani, zipangizo za nyumba ya Yehova zidzatengedwanso ku Babiloni posachedwa; pakuti akunenerani inu zonama. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndiponso ndinanena kwa ansembe ndi kwa anthu onsewa, kuti, Yehova atero: Musamvere mau a aneneri anu amene akunenerani inu, kuti, Taonani, zipangizo za nyumba ya Yehova zidzatengedwanso ku Babiloni posachedwa; pakuti akunenerani inu zonama. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 “Pambuyo pake ndidauza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti Chauta akunena kuti: Musaŵamvere aneneri anu amene amakuuzani kuti, ‘Ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta adzazibwezanso mwamsanga kuchokera ku Babiloni.’ Iwowo akungokuloserani zabodza. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Kenaka ndinawuza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti, “Yehova akuti: Musamvere aneneri amene akumanena kuti, ‘Posachedwapa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zibwera kuchokera ku Babuloni.’ Iwowo akunenera zabodza kwa inu. Onani mutuwo |