Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 27:15 - Buku Lopatulika

15 Pakuti sindinawatume iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupirikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Pakuti sindinawauma iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupirikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Sindidaŵatume ndine, ngakhale iwowo akuti amalosa m'dzina langa. Motero ndidzakupirikitsani, ndipo mudzaonongeka inuyo pamodzi ndi aneneri amene amakuloseraniwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Sindinawatume ngakhale iwo akulosera mʼdzina langa. Nʼchifukwa chake, ndidzakupirikitsani ndipo mudzawonongeka kotheratu, inu pamodzi ndi aneneri amene akunenera zabodza kwa inu.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 27:15
27 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatume iwo, sindinauze iwo, sindinanene nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi chinthu chachabe, ndi chinyengo cha mtima wao.


Ndipo iwe, Pasuri, ndi onse okhala m'nyumba mwako mudzanka kundende; ndipo udzafika ku Babiloni, ndi pamenepo udzafa, ndi pamenepo udzaikidwa, iwe, ndi mabwenzi ako onse, amene unawanenera mabodza.


Chifukwa chake Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo chowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwatulukira kunka ku dziko lonse.


Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanene ndi iwo, koma ananenera.


Ndamva chonena aneneri, amene anenera zonama m'dzina langa, kuti, Ndalota, ndalota.


pakuti iwo akunenerani inu zonama, kuti akuchotseni inu m'dziko lanu, kunka kutali kuti ndikupirikitseni inu, ndipo inu mudzathedwa.


Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.


Pakuti anenera kwa inu zonama m'dzina langa; sindinatume iwo, ati Yehova.


Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzatulutsidwa kunka kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo.


Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.


chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.


Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa