Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 27:13 - Buku Lopatulika

13 Mudzaferanji, iwe ndi anthu anu, ndi lupanga ndi njala, ndi mliri, monga wanena Yehova za mtundu umene ukana kumtumikira mfumu ya ku Babiloni?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Mudzaferanji, iwe ndi anthu anu, ndi lupanga ndi njala, ndi chaola, monga wanena Yehova za mtundu umene ukana kumtumikira mfumu ya ku Babiloni?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Nanga iweyo ndi anthu ako, muferenji ndi nkhondo, njala ndi mliri, zimene Chauta waopsera mtundu wina uliwonse wosatumikira mfumu ya ku Babiloni?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Nanga inu ndi anthu anu, muferenji ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, zimene Yehova waopsezera mtundu wina uliwonse umene sudzatumikira mfumu ya ku Babuloni?

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 27:13
11 Mawu Ofanana  

Koma wondichimwira apweteka moyo wake; onse akundida ine akonda imfa.


Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya.


Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m'mene ndidzawapirikitsiramo.


Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake.


Yehova atero, Iye wakukhala m'mzindawu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye wakutulukira kunka kwa Ababiloni adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wake ngati chofunkha, nadzakhala ndi moyo.


Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, chomwecho kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.


Ndipo adzatulutsira Ababiloni akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babiloni; ndipo mudzatenthetsa mzindawu ndi moto.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?


Koma wolungamayo akabwerera kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, ndi kuchita monga mwa zonyansa zonse azichita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena chimodzi cha zolungama zake zonse adzazichita chidzakumbukika m'kulakwa kwake analakwa nako, ndi m'kuchimwa kwake anachimwa nako; momwemo adzafa.


Tayani, ndi kudzichotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israele?


Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa