Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 27:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m'goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye ndi anthu ake, ndipo mudzakhala ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m'goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye ndi anthu ake, ndipo mudzakhala ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Mau okhaokhawo ndidauzanso Zedekiya mfumu ya ku Yuda, ndidati: Mugonjere ulamuliro wa mfumu ya ku Babiloni ndi kumaitumikira iyoyo pamodzi ndi anthu ake. Mukatero mudzapulumutsa moyo wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Uthenga womwewu ndinawuzanso Hezekiya mfumu ya Yuda. Ndinati, “Gonjerani mfumu ya ku Babuloni. Itumikireni iyoyo pamodzi ndi anthu ake ndipo mudzakhala ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 27:12
11 Mawu Ofanana  

Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phee osaopa zoipa.


Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya.


Iye amene akhala m'mzinda uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.


Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake.


Ndipo panali chaka chomwecho, poyamba Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda, chaka chachinai, mwezi wachisanu, kuti Hananiya mwana wa Azuri mneneri, amene anali wa ku Gibiyoni, ananena ndi ine m'nyumba ya Yehova, pamaso pa ansembe ndi pa anthu onse, kuti,


Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Ndathyola goli la mfumu ya ku Babiloni.


Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Ngati mudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mzindawu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu;


Musaope mfumu ya ku Babiloni, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndili ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m'dzanja lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa