Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 27:11 - Buku Lopatulika

11 Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m'dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m'dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Koma mtundu wina uliwonse umene udzagonjera mfumu ya ku Babiloni ndi kumaitumikira, ndidzausiya kuti ukhale m'dziko lake, kuti uzilima ndi kumakhala kumeneko,” akuterotu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma ngati mtundu wina uliwonse udzagonjera mfumu ya ku Babuloni ndi kuyitumukira, ndidzawusiya kuti ukhale mʼdziko lake kuti uzilima ndi kukhalamo, akutero Yehova.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 27:11
8 Mawu Ofanana  

Iye amene akhala m'mzinda uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.


Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m'goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye ndi anthu ake, ndipo mudzakhala ndi moyo.


Yehova atero kwa ine: Udzipangire zomangira ndi magoli, nuziike pakhosi pako;


Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake.


Yehova atero, Iye wakukhala m'mzindawu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye wakutulukira kunka kwa Ababiloni adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wake ngati chofunkha, nadzakhala ndi moyo.


Atero Ambuye Yehova, Pakusonkhanitsa nyumba ya Israele mwa mitundu ya anthu anabalalikamo, ndidzazindikirika Woyera mwaiwowa, pamaso pa amitundu; ndipo adzakhala m'dziko mwaomwao ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa