Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 27:10 - Buku Lopatulika

10 pakuti iwo akunenerani inu zonama, kuti akuchotseni inu m'dziko lanu, kunka kutali kuti ndikupirikitseni inu, ndipo inu mudzathedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 kakuti iwo akunenerani inu zonama, kuti akuchotseni inu m'dziko lanu, kunka kutali kuti ndikupirikitseni inu, ndipo inu mudzathedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ndithudi, amakuloserani zabodza, kotero kuti adani adzakuchotsani m'dziko lanu, kupita nanu kutali. Ndidzakupirikitsani ndipo mudzaonongeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Iwo akukuloserani zabodza kotero kuti adani adzakuchotsani mʼdziko lanu nʼkupita nanu ku dziko lakutali. Ndidzakupirikitsani ndi kukuwonongani kotheratu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 27:10
17 Mawu Ofanana  

Wanyanga usamlola akhale ndi moyo.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatume iwo, sindinauze iwo, sindinanene nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi chinthu chachabe, ndi chinyengo cha mtima wao.


Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zachabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.


Ndamva chonena aneneri, amene anenera zonama m'dzina langa, kuti, Ndalota, ndalota.


Musamvere mau a aneneri amene anena ndi inu, kuti, simudzamtumikira mfumu ya ku Babiloni; pakuti akunenerani zonama.


Pakuti sindinawatume iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupirikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.


Ndiponso ndinanena kwa ansembe ndi kwa anthu onsewa, kuti, Yehova atero: Musamvere mau a aneneri anu amene akunenerani inu, kuti, Taonani, zipangizo za nyumba ya Yehova zidzatengedwanso ku Babiloni posachedwa; pakuti akunenerani inu zonama.


Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Chomwecho ndidzathyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babiloni zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulichotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anachoka.


Chifukwa chake Yehova atero, Taona, Ine ndidzakuchotsa iwe kudziko; chaka chino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.


Pakuti mzinda uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiuchotse pamaso panga;


Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi mu Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?


Aneneri ako anakuonera masomphenya achabe ndi opusa; osawulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako, koma anakuonera manenero achabe ndi opambutsa.


Pamenepo anafika alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitse kumasulira kwake.


Pakuti aterafi anena zopanda pake, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto achabe, asangalatsa nazo zopanda pake; chifukwa chake ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa.


Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.


Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa