Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 26:23 - Buku Lopatulika

23 ndipo anamtulutsa Uriya mu Ejipito, nanka naye kwa Yehoyakimu mfumu; amene anamupha ndi lupanga, naponya mtembo wake m'manda a anthu achabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 ndipo anamtulutsa Uriya m'Ejipito, nanka naye kwa Yehoyakimu mfumu; amene anamupha ndi lupanga, naponya mtembo wake m'manda a anthu achabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Iwowo adakagwira Uriya ku Ejipito komweko, nkubwera naye kwa mfumu Yehoyakimu. Mfumuyo idalamula kuti Uriyayo aphedwe, ndipo mtembo wake adakauika ku manda a anthu wamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Iwo anakamutenga Uriya ku Igupto kuja nabwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Iye anamupha ndi lupanga ndipo mtembo wake anakawutaya ku manda a anthu wamba).

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 26:23
13 Mawu Ofanana  

Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita makolo ake.


Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.


Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.


Adzamuika monga kuika bulu, adzamkoka nadzamponya kunja kwa zipata za Yerusalemu.


Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosachimwa, ndi pa mzinda uwu, ndi pa okhalamo ake; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m'makutu anu.


Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wachifumu wa Davide; ndipo mtembo wake udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli chisanu.


Ndipo unayendayenda pakati pa mikango, nukhala msona, nuphunzira kugwira nyama, nulusira anthu.


ndipo anatumiza mnyamata, namdula mutu Yohane m'nyumba yandende.


amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse;


anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa,


Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao chilombo chokwera kutuluka m'chiphompho chakuya chidzachita nazo nkhondo, ndipo chidzazigonjetsa, ndi kupha izo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa