Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 26:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo panalinso munthu amene ananenera m'dzina la Yehova, Uriya mwana wake wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu; ndipo iye ananenera mzinda uwu ndi dziko lino monga mwa mau onse a Yeremiya;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo panalinso munthu amene ananenera m'dzina la Yehova, Uriya mwana wake wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu; ndipo iye ananenera mudzi uwu ndi dziko lino monga mwa mau onse a Yeremiya;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Padaalinso munthu wina amene ankalosa m'dzina la Chauta, dzina lake Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu. Iyeyo adaalosanso zodzagwera mzinda uno ndi dziko lino monga momwe adachitira Yeremiya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 (Panalinso munthu wina, Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriati-Yeyarimu, amene ankalosera mʼdzina la Yehova. Iyeyu analosera za mzinda uno ndi dziko lino monga mmene wachitira Yeremiya.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 26:20
9 Mawu Ofanana  

Pali Yehova Mulungu wanu, ngati kuli mtundu umodzi wa anthu, kapena ufumu, kumene mbuye wanga sananditumeko kukufunani, ndipo pakunena iwo, Palibe iye, analumbiritsa ufumu umene ndi mtundu umene kuti sanakupezeni.


Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita makolo ake.


Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.


Ndipo akulu anati kwa Baruki, Pita, nubisale iwe ndi Yeremiya; munthu yense asadziwe kumene muli.


Kiriyati-Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yao.


Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kunka kumwera, kuchokera kuphiri pokhala patsogolo pa Betehoroni, kumwera kwake; ndi matulukiro ake anali ku Kiriyati-Baala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mzinda wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo.


Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumizinda yao tsiku lachitatu. Koma mizinda yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.


Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-Yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.


Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikulu mu Kiriyati-Yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israele linalirira Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa