Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 26:18 - Buku Lopatulika

18 Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 “Nthaŵi imene Hezekiya anali mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosa, ndipo adauza anthu onse a ku Yuda kuti Chauta Wamphamvuzonse akuti, “ ‘Ziyoni adzalimidwa ngati munda. Yerusalemu adzasanduka bwinja, phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 “Mʼmasiku a Hezekiya mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosera. Iye ankawuza anthu kuti Yehova Wamphamvuzonse akuti, “ ‘Ziyoni adzatipulidwa ngati munda, Yerusalemu adzasanduka bwinja, ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 26:18
13 Mawu Ofanana  

Sunamva kodi kuti Ine ndinachichita kale lomwe, ndi kuchipanga masiku akalekale? Tsopano ndachifikitsa kuli iwe, uzikhala wakupasula mizinda yamalinga ikhale miunda ya mabwinja.


Koma Hezekiya anadzichepetsa m'kudzikuza kwa mtima wake, iye ndi okhala mu Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzere masiku a Hezekiya.


Nanena iye pamaso pa abale ake ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikuchitanji Ayuda ofookawa? Adzimangire linga kodi? Adzapereka nsembe kodi? Adzatsiriza tsiku limodzi kodi? Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa?


Mulungu, akunja alowa m'cholowa chanu; anaipsa Kachisi wanu woyera; anachititsa Yerusalemu bwinja.


Iwe phiri langa la m'munda, ndidzapereka chuma chako ndi zosungidwa zako zikafunkhidwe, ndi misanje yako, chifukwa cha tchimo, m'malire ako onse.


Ndipo Babiloni adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, chizizwitso, chotsonyetsa, wopanda okhalamo.


Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.


Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.


Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mzinda wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa