Yeremiya 26:15 - Buku Lopatulika15 Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosachimwa, ndi pa mzinda uwu, ndi pa okhalamo ake; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m'makutu anu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosachimwa, ndi pa mudzi uwu, ndi pa okhalamo ake; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m'makutu anu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Koma tsono mudziŵe kuti mukangondipha, ndiye kuti inuyo pamodzi ndi mzinda uno ndi anthu onse okhalamo, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi, nzoona kuti Chauta ndiye adandituma kwa inu, kuti mumve zonse ndikunenazi.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Komatu dziwani kuti ngati mundipha, inu pamodzi ndi mzinda uno ndi onse amene amakhala muno, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi Yehova anandituma kuti ndidzayankhule mawu onsewa inu mukumva.” Onani mutuwo |