Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 24:5 - Buku Lopatulika

5 Chifukwa Yehova, Mulungu wa Israele, atero, Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira am'nsinga a Yuda, amene ndawachotsera m'malo muno kunka kudziko la Ababiloni, kuwachitira bwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Chifukwa Yehova, Mulungu wa Israele, atero, Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira am'nsinga a Yuda, amene ndawachotsera m'malo muno kunka kudziko la Ababiloni, kuwachitira bwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 “Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti, Akapolo a ku Yuda amene ndidaŵachotsa ku malo ano, kupita nawo ku dziko la Ababiloni, ndikuŵafanizira ndi nkhuyu zabwinozi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 “Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Anthu a ku Yuda amene ndinawachotsa ku malo ano nʼkupita nawo ku ukapolo ku dziko la Ababuloni ndikuwafanizira ndi nkhuyu zabwinozi.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 24:5
21 Mawu Ofanana  

Ndisanazunzidwe ndinasokera; koma tsopano ndisamalira mau anu.


Kundikomera kuti ndinazunzidwa; kuti ndiphunzire malemba anu.


Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,


Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.


Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m'ndende, amene ndachotsa mu Yerusalemu kunka ku Babiloni.


Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, kwa am'nsinga onse, amene ndinawatenga ndende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni:


Chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani kumitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani muchoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israele.


kuti ayende m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.


Ndiponso pali ichinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kuthyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wao.


Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani.


Nkhosa zanga zimva mau anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine.


Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.


Koma ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye.


koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?


amene anakudyetsani m'chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;


Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa