Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 23:9 - Buku Lopatulika

9 Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; chifukwa cha Yehova, ndi chifukwa cha mau ake opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; chifukwa cha Yehova, ndi chifukwa cha mau ake opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Kunena za aneneri, mtima wanga wasweka, m'nkhongono mwachita kuti zii! Ndakhala ngati munthu woledzera, munthu wosokonezeka ndi vinyo, chifukwa cha Chauta ndi mau ake oyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kunena za aneneri awa: Mtima wanga wasweka; mʼnkhongono mwati zii. Ndakhala ngati munthu woledzera, ngati munthu amene wasokonezeka ndi vinyo, chifukwa cha Yehova ndi mawu ake opatulika.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 23:9
21 Mawu Ofanana  

Mwaonetsa anthu anu zowawa, mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.


Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.


Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efuremu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'chigwa cha nthaka yabwino.


Khalani ndi kudabwa; sangalalani ndi kukhala akhungu; iwo aledzera, koma si ndi vinyo, ali dzandidzandi; koma si ndi chakumwa chaukali.


Chifukwa chake imva ichi tsopano, iwe wovutidwa ndi woledzera koma si ndi vinyo ai;


Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.


Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.


Ndipo panali, pamene anamva mau onse, anaopa nayang'anana wina ndi mnzake, nati kwa Baruki, Tidzamfotokozeratu mfumu mau awa onse.


aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?


Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Wandidzaza ndi zowawa, wandikhutitsa chivumulo.


Atero Ambuye Yehova, Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu waowao, chinkana sanaone kanthu.


Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mzinda, pakati pa Yerusalemu, nulembe chizindikiro pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.


iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu aliyense ali nacho chizindikiro, ndipo muyambe pamalo anga opatulika. Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba.


Ndipo ine Daniele ndinakomoka ndi kudwala masiku ena; pamenepo ndinauka ndi kuchita ntchito ya mfumu; ndipo ndinadabwa nao masomphenyawo, koma panalibe wakuwazindikiritsa.


Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamau, m'mafupa mwanga mudalowa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.


Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, uchimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa