Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 23:12 - Buku Lopatulika

12 Chifukwa chake njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzachotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Chifukwa chake njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzachotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Nchifukwa chake njira zao zidzakhala zoterera. Adzaŵapirikitsira kumdima kumene akagwe. Ndidzaŵaonetsa ndoza pa nthaŵi ya chilango chao,” akuterotu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera; adzawapirikitsira ku mdima ndipo adzagwera kumeneko. Adzaona zosaona mʼnthawi ya chilango chawo,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 23:12
18 Mawu Ofanana  

Adzamkankha achoke kukuunika alowe kumdima; adzampirikitsa achoke m'dziko lokhalamo anthu.


Njira yao ikhale ya mdima ndi yoterera, ndipo mngelo wa Yehova awalondole.


Indedi muwaika poterera, muwagwetsa kuti muwaononge.


Sadziwa, ndipo sazindikira; amayendayenda mumdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.


Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kunka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga chifukwa cha kuchimwa kwao.


Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa.


nadzayang'ana padziko, koma taonani, nkhawa ndi mdima, kuziya kwa nsautso; ndi mdima woti bii udzaingitsidwa.


ndipo sadzakhala nao otsalira; pakuti ndidzatengera choipa pa anthu a ku Anatoti, chaka cha kulangidwa kwao.


Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanaphunthwe pa mapiri achizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Iye asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii.


Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.


Iphani ng'ombe zamphongo zake zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! Pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao.


Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.


Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawalera wokha? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?


Wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wao aipa koposa mpanda waminga; tsiku la alonda ako la kulangidwa kwako lafika, tsopano kwafika kuthedwa nzeru kwao.


Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.


Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.


Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake.


mafunde oopsa a nyanja, akuwinduka thovu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa