Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 22:6 - Buku Lopatulika

6 Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Giliyadi, ndi mutu wa Lebanoni; koma ndidzakuyesa iwe chipululu, ndi mizinda yosakhalamo anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Giliyadi, ndi mutu wa Lebanoni; koma ndidzakuyesa iwe chipululu, ndi midzi yosakhalamo anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Naŵa mau a Chauta onena za nyumba ya mfumu ya ku Yuda: “Ngakhale iwe ndimakukonda ngati Giliyadi, kapena ngati nsonga ya phiri la Lebanoni, komabe ndidzakusandutsa chipululu, mzinda wopanda anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Pakuti zimene Yehova akunena za nyumba yaufumu ya mfumu ya ku Yuda ndi izi: “Ngakhale iwe uli ngati Giliyadi kwa Ine, ngati msonga ya phiri la Lebanoni, komabe ndidzakusandutsa chipululu, ngati mizinda yopanda anthu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:6
26 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndi ngamira zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi mure alinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito.


Dziko la zipatso, likhale lakhulo, chifukwa cha choipa cha iwo okhalamo.


Taona, wakongola, bwenzi langa, namwaliwe, taona, wakongola; maso ako akunga a nkhunda patseri pa chophimba chako. Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi, zooneka paphiri la Giliyadi.


Miyendo yake ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira, zogwirika m'kamwa mwa golide: Maonekedwe ake akunga Lebanoni, okometsetsa ngati mikungudza.


Pakuti mzinda wotchingidwa uli pa wokha, mokhalamo mwa bwinja, ndi mosiyidwa ngati chipululu; mwanawang'ombe adzadya kumeneko, nadzagonako pansi, nadzamaliza nthambi zake.


Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magaleta anga ine ndafika kunsonga za mapiri, kumbali za Lebanoni; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pake penipeni, kunkhalango ya munda wake wobalitsa.


Pompo ndinati ine, Ambuye mpaka liti? Ndipo anayankha, Mpaka mizinda ikhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda munthu, ndi dziko likhala bwinja ndithu,


Ndipo za nyumba ya mfumu ya Yuda, tamvani mau a Yehova:


Ndipo ndidzakulangani inu monga mwa chipatso cha ntchito zanu, ati Yehova; ndipo ndidzayatsa moto m'nkhalango mwake, ndipo udzatha zonse zomzungulira iye.


Pali Ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wake wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya padzanja langa lamanja, ndikadachotsa iwe kumeneko;


Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.


Alalikira chipasuko chilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsalu zanga zotchinga m'kamphindi.


Mkango wakwera kutuluka m'nkhalango mwake, ndipo waononga amitundu ali panjira, watuluka m'mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti mizinda yako ipasuke mulibenso wokhalamo.


amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, chipululu, dziko louma, bwinja.


Ndipo ndidzaletsa m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, mau akukondwa ndi mau akusekera, ndi mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi; pakuti dziko lidzasanduka bwinja.


Kodi mulibe vunguti mu Giliyadi? Kodi mulibe sing'anga m'menemo; analekeranji kuchira mwana wamkazi wa anthu anga?


Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Tsegula pa makomo ako Lebanoni, kuti moto uthe mikungudza yako.


Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.


Ndioloketu, ndilione dziko lokomali lili tsidya la Yordani, mapiri okoma aja, ndi Lebanoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa