Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 22:5 - Buku Lopatulika

5 Koma ngati simudzamva mau amenewa, Ine ndilumbira, pali Ine mwini, ati Yehova, nyumba iyi idzakhala yabwinja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma ngati simudzamva mau amenewa, Ine ndilumbira, pali Ine mwini, ati Yehova, nyumba iyi idzakhala yabwinja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Koma ngati sudzamvera mau anga, ndikulumbira pali Ine ndemwe, kuti nyumba imeneyi idzasanduka bwinja!’ ” Akuterotu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Koma ngati sumvera malamulo awa, akutero Yehova, ndikulumbira pali Ine ndemwe kuti nyumba ino yaufumu idzasanduka bwinja.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:5
22 Mawu Ofanana  

nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikanize mwana wako, mwana wako yekha,


Koma mukabwerera inu, ndi kusiya malemba anga, ndi malamulo anga, amene ndaika pamaso panu, ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuilambira;


Ndi munthu yense wakupita pa nyumba iyi yaitali adzadabwa nayo, nadzati, Yehova anatero ndi dziko lino ndi nyumba ino chifukwa ninji?


Ndipo adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wa makolo ao amene anawatulutsa m'dziko la Ejipito, nagwira milungu ina, nailambira ndi kuitumikira; chifukwa chake anawagwetsera choipa ichi chonse.


Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga.


koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.


Ndachoka kunyumba yanga, ndasiya cholowa changa; ndapereka wokondedwa wa mtima wanga m'dzanja la adani.


Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zakezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.


Ndipo iwe uziti kwa iwo, Yehova atero: Ngati simudzandimvera Ine kuyenda m'chilamulo changa, chimene ndachiika pamaso panu,


Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.


Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda okhala m'dziko la Ejipito: Taonani, ndalumbira, Pali dzina langa lalikulu, ati Yehova, kuti dzina langa silidzatchulidwanso m'kamwa mwa munthu aliyense wa Yuda m'dziko la Ejipito, ndi kuti, Pali Yehova Mulungu.


Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zake zachifumu; m'mwemo ndidzapereka mzinda, ndi zonse zili m'menemo.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.


Ndipo adawalumbirira ayani kuti asalowe mpumulo wake?


Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa Iye yekha,


Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa olowa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa