Yeremiya 22:26 - Buku Lopatulika26 Ndipo ndidzakutulutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m'dziko lina, limene sunabadwiremo; m'menemo udzafa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Ndipo ndidzakutulutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m'dziko lina, limene sunabadwiramo; m'menemo udzafa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa26 Ndidzakupititsa ku dziko lina pamodzi ndi mai wako amene adakubala. Simudabadwire kumeneko, komabe nonsenu mudzafera kumeneko. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Iwe pamodzi ndi amayi ako amene anakubereka ndidzakupititsani ku dziko lachilendo. Ngakhale inu simunabadwire kumeneko, komabe mudzafera komweko. Onani mutuwo |
Ndipo kunali chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri cha kumtenga ndende Yehoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya Babiloni anamuweramutsa mutu wake wa Yehoyakini mfumu ya Yuda atuluke m'kaidi, chaka cholowa iye ufumu wake;