Yeremiya 22:25 - Buku Lopatulika25 ndipo ndidzakupereka iwe m'dzanja la iwo amene afuna moyo wako, m'dzanja la iwo amene uwaopa, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, m'dzanja la Ababiloni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 ndipo ndidzakupereka iwe m'dzanja la iwo amene afuna moyo wako, m'dzanja la iwo amene uwaopa, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, m'dzanja la Ababiloni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Ndidzakupereka kwa anthu ofuna kukupha, amene umaŵaopa, ndiye kuti kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi anthu ake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Ndidzakupereka kwa amene akufuna kukupha, amene iwe umawaopa. Ndidzakupereka kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni ndi anthu ake. Onani mutuwo |
Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.