Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 22:22 - Buku Lopatulika

22 Mphepo idzadyetsa abusa ako onse, ndipo mabwenzi ako adzalowa m'ndende; ntheradi udzakhala ndi manyazi ndi kunyazitsidwa chifukwa cha choipa chako chonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Mphepo idzadyetsa abusa ako onse, ndipo mabwenzi ako adzalowa m'ndende; ntheradi udzakhala ndi manyazi ndi kunyazitsidwa chifukwa cha choipa chako chonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse, ndipo amene munkaŵadalira adzatengedwa ukapolo. Tsono mudzanyozedwa, mudzachita manyazi, chifukwa cha zolakwa zanu zochuluka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse, ndipo abwenzi anu adzatengedwa ku ukapolo. Pamenepo mudzachita manyazi ndi kunyozedwa chifukwa cha zoyipa zanu zonse.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:22
24 Mawu Ofanana  

Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse zili ngati chovala chodetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi;


Pakuti abusa apulukira, sanafunsire kwa Yehova; chifukwa chake sanapindule; zoweta zao zonse zabalalika.


Abusa ambiri aononga munda wanga wampesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu.


Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? Udzachitanso manyazi ndi Ejipito monga unachita manyazi ndi Asiriya.


Koma udzatuluka kwa iyenso, manja ako pamutu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.


Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? Ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.


Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.


Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka.


Nanga iwe, udzachita chiyani pamene udzafunkhidwa? Ngakhale udziveka ndi zofiira, ngakhale udziveka ndi zokometsera zagolide, ngakhale udzikuzira maso ako ndi kupaka, udzikometsera pachabe; mabwenzi adzakunyoza adzafuna moyo wako.


ndipo aneneri adzasanduka mphepo, ndipo mwa iwo mulibe mau; chomwecho chidzachitidwa ndi iwo.


Kodi autsa mkwiyo wanga? Ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao?


Efuremu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse achulukitsa mabodza ndi chipasuko, ndipo achita pangano ndi Asiriya, natenga mafuta kunka nao ku Ejipito.


Chinkana abala mwa abale ake, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kuchokera kuchipululu; ndi gwero lake lidzaphwa, ndi kasupe wake adzauma, adzafunkha chuma cha akatundu onse ofunika.


Mphepo yamkulunga m'mapiko ake, ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zao.


Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga padzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.


Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa