Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 22:19 - Buku Lopatulika

19 Adzamuika monga kuika bulu, adzamkoka nadzamponya kunja kwa zipata za Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Adzamuika monga kuika bulu, adzamkoka nadzamponya kunja kwa zipata za Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Adzamuika ngati bulu basi, kuchita kumguguza nkukamtaya kuseri kwa zipata za Yerusalemu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Adzayikidwa ngati bulu, kuchita kumuguguza ndi kukamutaya kunja kwa zipata za Yerusalemu.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:19
13 Mawu Ofanana  

chifukwa chake, taona ndidzafikitsa choipa pa nyumba ya Yerobowamu, ndi kugulula mwana wamwamuna yense wa Yerobowamu womangika ndi womasuka mu Israele, ndipo ndidzachotsa psiti nyumba yonse ya Yerobowamu, monga munthu achotsa ndowe kufikira idatha yonse.


Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Zebida mwana wa Pedaya wa Ruma.


Nagona Yehoyakimu ndi makolo ake, ndipo Yehoyakini mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Namuka iwo kuti amuike; koma sanapezeko kanthu kena koma bade, ndi mapazi, ndi zikhato za manja.


Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwera kuyambana naye, nammanga ndi matangadza kumuka naye ku Babiloni.


Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;


Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agalu akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zilombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.


Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wachifumu wa Davide; ndipo mtembo wake udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli chisanu.


koma pita iwe, nuwerenge mu mpukutu umene ndakulembetsa, mau a Yehova m'makutu a anthu m'nyumba ya Yehova tsiku lakusala kudya; ndiponso udzawawerenga m'makutu a Ayuda onse amene atuluka m'mizinda yao.


ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.


Pamenepo mitundu ya anthu inadzipereka kuukola kuchokera kumaiko a kumbali zonse, niuphimba ndi ukonde wao, nugwidwa uwu m'mbuna mwao.


Udzagwa kuthengo, koyera, pakuti ndanena ndine, ati Ambuye Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa