Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 22:18 - Buku Lopatulika

18 Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda: Sadzamlira iye, kuti, Kalanga ine mbale wanga! Kapena, Kalanga ine mlongo wanga! Sadzamlira, kuti, Kalanga ine mbuye! Kapena, Kalanga ine ulemerero wake!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda: Sadzamlira iye, kuti, Kalanga ine mbale wanga! Kapena, Kalanga ine mlongo wanga! Sadzamlira, kuti, Kalanga ine mbuye! Kapena, Kalanga ine ulemerero wake!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Nchifukwa chake Chauta ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, akuti, “Sipadzakhala womulira munthu ameneyo kuti, ‘Kalanga ine, mbale wanga!’ Kapena kuti, ‘Kalanga ine, mlongo wanga!’ Sipadzakhala womulira kuti, ‘Kalanga ine, mbuye wanga!’ Kapena kuti, ‘Kalanga ine, mfumu yanga.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti, “Anthu sadzamulira maliro kapena kunena kuti, ‘Kalanga ine, mʼbale wanga! Kalanga ine mlongo wanga! Anthu ake sadzamulira maliro kuti, Kalanga ine, mbuye wathu! Taonani ulemerero wake wapita!’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:18
17 Mawu Ofanana  

Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Yonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu aakazi.


Ndipo mtembo wake anauika m'manda a iye mwini, namlira iwo maliro, nati, Mayo, mbale wanga!


Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Zebida mwana wa Pedaya wa Ruma.


Natulutsa chifanizocho m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nachitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nachipera chikhale fumbi, naliwaza fumbi lake pa manda a ana a anthu.


Nagona Yehoyakimu ndi makolo ake, ndipo Yehoyakini mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndi ana a Yosiya: woyamba Yohanani, wachiwiri Yehoyakimu, wachitatu Zedekiya, wachinai Salumu.


Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba mu Israele; taonani, zilembedwa mu Nyimbo za Maliro.


Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.


Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi.


Akulu ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzachita maliro ao, sadzadzicheka, sadzadziyeseza adazi, chifukwa cha iwo;


Ndipo za nyumba ya mfumu ya Yuda, tamvani mau a Yehova:


Musamlirire wakufa, musachite maliro ake; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao.


koma kumene anamtengera iye ndende, kumeneko adzafa, ndipo sadzaonanso dziko ili.


udzafa ndi mtendere; ndipo adzawambika iwe monga anawambika makolo ako, mafumu akale usanakhale iwe; ndipo adzakulirira iwe, kuti, Kalanga ine ambuye! Pakuti ndanena mau, ati Yehova.


Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wachifumu wa Davide; ndipo mtembo wake udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli chisanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa