Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 22:14 - Buku Lopatulika

14 amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikulu, nadziboolera mazenera; navundikira tsindwi lam'kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikulu, nadziboolera mazenera; navundikira chindwi lam'kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Munthuyo amanena kuti, ‘Ndidzadzimangira nyumba yaikulu, ya zipinda zam'mwamba zikuluzikulu, ndidzaikamo mawindo, ndi kukhomamo matabwa a mkungudza, ndipo ndidzaipaka utoto wofiira.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Munthuyo amati, ‘Ndidzadzimangira nyumba yayikulu ya zipinda zikuluzikulu zamʼmwamba.’ Kotero ndidzapanga mazenera akuluakulu, ndi kukhomamo matabwa a mkungudza ndi kukongoletsa ndi makaka ofiira.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:14
13 Mawu Ofanana  

mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndilikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu lili m'kati mwa nsalu zotchinga.


M'nyumba yaikulu tsono anatchinga ndi mitengo yamlombwa, imene anaikuta ndi golide wabwino, nalembapo ngati migwalangwa ndi maunyolo.


Wokonda ndeu akonda kulakwa; ndipo wotalikitsa khomo lake afunafuna kuonongeka.


Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.


Mitanda ya nyumba zathu nja mikungudza, ndi mapaso athu nga mlombwa.


Ndipo anthu onse adzadziwa, ngakhale Efuremu ndi okhala mu Samariya, amene anena m'kunyada ndi m'kukula kwa mtima,


Ndipo anaonjeza zigololo zake, naona amuna olembedwa pakhoma, zithunzithunzi za Ababiloni olembedwa ndi kundwe;


Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga?


Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zake zachifumu; m'mwemo ndidzapereka mzinda, ndi zonse zili m'menemo.


Kodi imeneyi ndiyo nthawi yakuti inu nokha mukhala m'nyumba zanu zochingidwa m'katimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka?


Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa