Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 22:11 - Buku Lopatulika

11 Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m'malo mwake mwa Yosiya atate wake, amene anatuluka m'malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iliyonse;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m'malo mwake mwa Yosiya atate wake, amene anatuluka m'malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iliyonse;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Paja Salumu, mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, adaloŵa m'malo mwa atate ake pa mpando waufumu umene adausiya. Tsono ponena za amene uja Chauta akuti, “Iyeyo sadzabwereranso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Pakuti zimene Yehova akunena za Yehowahazi mwana wa Yosiya, amene anatenga mpando waufumu wa Yuda mʼmalo mwa abambo ake koma nʼkuwusiya ndi izi: “Iye sadzabwereranso.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:11
10 Mawu Ofanana  

Masiku ake Farao Neko mfumu ya Aejipito anakwerera mfumu ya Asiriya ku mtsinje wa Yufurate; ndipo mfumu Yosiya anatuluka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona.


Ndipo anyamata ake anamtengera wakufa m'galeta, nabwera naye ku Yerusalemu kuchokera ku Megido, namuika m'manda akeake. Ndipo anthu a m'dziko anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namdzoza, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake.


Yehowahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu miyezi itatu mu Yerusalemu ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.


Ndipo Farao Neko analonga ufumu Eliyakimu mwana wa Yosiya, m'malo mwa Yosiya atate wake, nasanduliza dzina lake likhale Yehoyakimu; koma anapita naye Yehowahazi, nafika iye mu Ejipito, nafa komweko.


Ndi ana a Yosiya: woyamba Yohanani, wachiwiri Yehoyakimu, wachitatu Zedekiya, wachinai Salumu.


Pamenepo akulu ena a ana a Efuremu, Azariya mwana wa Yohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, ndi Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, anaukira aja ofuma kunkhondo,


Namuka Hilikiya ndi iwo aja adawauza mfumu kwa Hulida mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira wosunga zovala, amene anakhala mu Yerusalemu m'dera lachiwiri, nanena naye mwakuti.


Koma kudziko kumene moyo wao ukhumba kubwerera, kumeneko sadzabwerako.


Mau a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa