Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 21:9 - Buku Lopatulika

9 Iye amene akhala m'mzinda uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Iye amene akhala m'mudzi uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Aliyense wotsala mu mzinda uno adzafa ndi nkhondo, njala kapena mliri. Koma aliyense amene adzadzipereka kwa Ababiloni amene akuzingani ndi zithando zankhondo aja, ameneyo adzakhala ndi moyo, adzapulumuka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzaphedwa ndi lupanga, njala kapena mliri. Koma aliyense amene apite kukadzipereka kwa Ababuloni amene akuzinganiwa adzakhala ndi moyo, adzapulumuka.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 21:9
12 Mawu Ofanana  

Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi mliri.


Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.


Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi mliri mwa iwo, mpaka athedwa m'dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo ao.


Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m'dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo.


Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m'goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye ndi anthu ake, ndipo mudzakhala ndi moyo.


Mudzaferanji, iwe ndi anthu anu, ndi lupanga ndi njala, ndi mliri, monga wanena Yehova za mtundu umene ukana kumtumikira mfumu ya ku Babiloni?


Yehova atero, Iye wakukhala m'mzindawu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye wakutulukira kunka kwa Ababiloni adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wake ngati chofunkha, nadzakhala ndi moyo.


Yehova atero, Mzindawu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.


Pakuti ndidzakupulumutsatu ndipo sudzagwa ndi lupanga, koma udzakhala nao moyo wako ngati chofunkha, pakuti wandikhulupirira Ine, ati Yehova.


Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, ati Yehova: koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati chofunkha m'malo monse m'mene mupitamo.


Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa