Yeremiya 21:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mudzi uwu amene asiyidwa ndi chaola, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Pambuyo pake ndidzapititsa ku ukapolo Zedekiya mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, ndi anthu otsala mumzindamu opulumuka ku mliri, ku njala ndi ku nkhondo. Ndidzaŵapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndiponso kwa adani ao amene akufuna kuŵapha. Adzaŵaphadi ndi lupanga, sadzaŵamvera chisoni kapena chifundo.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Pambuyo pake, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi anthu a mu mzinda muno amene adzapulumuke pa nthawi ya mliri, lupanga ndi njala kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi kwa adani awo amene ankafuna kuwapha. Iye adzawapha ndi lupanga. Sadzawachitira chifundo kapena kuwamvera chisoni kapenanso kuwakomera mtima.’ Onani mutuwo |
Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe choopsa cha kwa iwe mwini, ndi kwa abwenzi ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babiloni, nadzawapha ndi lupanga.