Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 21:10 - Buku Lopatulika

10 Pakuti ndaika nkhope yanga pa mzinda uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pakuti ndaika nkhope yanga pa mudzi uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Mzinda umenewu ndatsimikiza kuti ndidzauchita zoipa osati zabwino ai. Udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babiloni ndipo iyeyo adzautentha ndi moto.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ine ndatsimikiza kuchitira mzinda uno choyipa osati chabwino, akutero Yehova. Udzaperekedwa mʼdzanja la mfumu ya ku Babuloni, ndipo iyeyo adzawutentha ndi moto.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 21:10
26 Mawu Ofanana  

Ndipo anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zake zonse zachifumu ndi moto, naononga zipangizo zake zonse zokoma.


Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao padziko lapansi.


Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zakezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.


pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.


Adza kumenyana ndi Ababiloni, koma adzangozidzaza ndi mitembo ya anthu, amene ndawapha m'mkwiyo wanga ndi mu ukali wanga, amene ndabisira mzinda uno nkhope yanga chifukwa cha zoipa zao zonse.


Yehova Mulungu wa Israele atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mzindawu m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzautentha ndi moto;


Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo kumzinda uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.


Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Ngati mudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mzindawu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu;


koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.


Ndipo adzatulutsira Ababiloni akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babiloni; ndipo mudzatenthetsa mzindawu ndi moto.


Yehova atero, Mzindawu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.


Pita, ukanene kwa Ebedemeleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taona, ndidzafikitsira mzinda uwu mau anga kuusautsa, osauchitira zabwino; ndipo adzachitidwa pamaso pako tsiku lomwelo.


Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.


Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzayang'anitsa nkhope yanga pa inu ndikuchitireni inu choipa, ndidule Yuda yense.


Taonani, ndiwayang'anira kuwachitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m'dziko la Ejipito adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao.


ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto.


Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzatuluka kumoto, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse.


Pamenepo uukhazike pa makala ake opanda kanthu m'menemo, kuti utenthe, nuyake mkuwa wake; ndi kuti chodetsa chake chisungunuke m'mwemo, kuti dzimbiri lake lithe.


Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.


koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zachifumu za mu Yerusalemu.


Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwachitira choipa, si chokoma ai.


Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa