Yeremiya 20:5 - Buku Lopatulika5 Ndiponso ndidzapereka chuma chonse cha mzinda uwu, ndi zaphindu zake zonse, ndi zinthu zake zonse za mtengo wake, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m'manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babiloni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndiponso ndidzapereka chuma chonse cha mudzi uwu, ndi zaphindu zake zonse, ndi zinthu zake zonse za mtengo wake, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m'manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babiloni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Chuma chonse chamumzindamu, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zonse za mtengo wapatali ndi chuma cha mafumu a ku Yuda, zonsezo ndidzazipereka kwa adani ao. Iwowo adzafunkha zimenezi ndi kupita nazo ku Babiloni. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Ndidzapereka kwa adani awo chuma chonse cha mu mzinda uno, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zake zonse za mtengowapatali ndiponso katundu yense wa mafumu a ku Yuda. Iwo adzazitenga monga zinthu zolanda ku nkhondo ndi kupita nazo ku Babuloni. Onani mutuwo |